WHDL - 00015106
About Site Language
WHDL is viewable in multiple languages. Use the pull-down menu to select a language to view the site.
I changed my language, but I’m still seeing resources in the other languages?
If a resource or text has not been translated into your selected language, it will appear in the initially added language. We are always looking for help translating these resources. If you can help, contact us!
WHDL - 00015106
MALONJE KWA OPHUNZIRA
Tsopano ndinu Mkhristu. Mukufunika kuphunzira kukula ngati Mkhristu. Muphunzira maphunziro asanu ndi atatu a kukula ngati Mkhristu.
Phunzirani phunziro lililonse pa nokha. Werengani Baibulo. Yankhani mafunso m’mene mungathere. Kenako, kumanani ndi m’phunzitsi kapena m’busa wanu. Adzayankha mafunso amene simukuwadziwa. Akakuthandizani kumvetsa maphunziro.
Mudzapeza vesi la Baibulo loloweza mu phunziro lililonse. Lowezani. Mavesi akuthandizani kukula Mkhristu.
Nthawi zina, mudzaona mawu olembedwa akuda kwambiri, ngati apa. Awa ndi mawu kapena ziganizo zifupizifupi zimene zikhoza kukhala za chilendo. Pamapeto pa phunziro lililonse, mudzapeza mndandanda wa mawu okhala ndi kufotokozera kwake mwa chidule.
Mulungu amakukondani kwambiri. Akufuna akhale Mulungu wanu. Akufuna inu muphunzire za iye. Mukhoza kuyankhula ndi Mulungu. Mukhoza kumupempha kuti akuthandinzeni. Adzakuthandizani kumvetsetsa. Adzakuthandizani kuphunzira.
MALONJE KWA M’PHUNZITSI
Perekani buku ili kwa Mkhristu wa tsopano pa nthawi ya kutembenuka mtima kwake, kapena akangotembenuka kumene. Limbikitsani munthuyo kuwerenga maphunziro ndi kuyankha mafunso m’mene angathere. Funsani munthuyo kuchita phunziro limodzi lokha pa nthawi. Yesetsani kukhazikitsa nthawi sabata iliyonse kukumana ndi ophunzira kuti mukambirane phunziro.
Ngati ophunzira sangawerenge phunziro pa wokha, khazikitsani nthawi imene mungawerenge ndi kukambirana maphunziro pamodzi. Pamene ziri zofunikira kuchita phunziro limodzi pa nthawi, zikhoza kukhala zofunikira kukhala ndi zigawo zophunzira zoposera kamodzi ndi phunziro lililonse. Thandizani ophunzira pa kuyang’ana malemba mu Baibulo. Yankhani mafunso pamodzi, kuwonetsetsa kuti ophunzira wamvetsetsa phunziro musanapite pa phunziro lina. (Mayankho olondola akhoza kupezeka mu Mawu owonjenzera.)
(English: Basic Bible Studies for New and Growing Christians)
You have permission to view this content and print a copy for personal use only. Permission to print multiple quantities of this resource is expressly forbidden.Contact the publisher for any translation or publishing use, which includes digital use in any and all media.